Aefeso
2 Ndiponso, Mulungu anapangitsa inuyo kukhala amoyo pamene munali akufa chifukwa cha zolakwa zanu ndi machimo anu.+ 2 Munali kuyenda m’zimenezo mogwirizana ndi nthawi*+ za m’dzikoli, momveranso wolamulira+ wa mpweya umene umalamulira zochita za anthu. Mpweya umenewu, kapena kuti kaganizidwe kameneka,+ tsopano kakugwira ntchito mwa ana a kusamvera.+ 3 Inde, tonsefe pa nthawi inayake pamene tinali pakati pawo, tinali kukhala motsatira zilakolako za thupi lathu.+ Tinali kuchita zofuna za thupi+ ndi maganizo, ndipo mwachibadwa tinali ana oyenera kulandira mkwiyo wa Mulungu,+ mofanana ndi ena onse. 4 Koma Mulungu, amene ndi wachifundo chochuluka,+ mwachikondi chake chachikulu chimene anatikonda nacho,+ 5 anatikhalitsa amoyo pamodzi ndi Khristu, ngakhale kuti tinali akufa m’machimo,+ (pakuti inu mwapulumutsidwa chifukwa cha kukoma mtima kwakukulu)+ 6 ndipo anatikweza+ pamodzi, ndi kutikhazika pamodzi m’malo akumwamba+ mogwirizana ndi Khristu Yesu. 7 Anachita zimenezi kuti mu nthawi* zimene zikubwera+ padzasonyezedwe chuma chopambana+ cha kukoma mtima kwake kwakukulu kumene anatisonyeza mogwirizana+ ndi Khristu Yesu.
8 Mwa kukoma mtima kwakukulu kumeneku, ndithudi mwapulumutsidwa kudzera m’chikhulupiriro,+ osati mwa inu nokha,+ koma monga mphatso ya Mulungu.+ 9 Si chifukwanso cha ntchito ayi,+ kuti munthu asakhale ndi chifukwa chodzitamandira.+ 10 Pakuti ndife ntchito ya manja ake,+ ndipo tinalengedwa+ mogwirizana+ ndi Khristu Yesu kuti tichite ntchito zabwino,+ zimene Mulungu anakonzeratu+ kuti tiyendemo.
11 Chotero nthawi zonse muzikumbukira kuti poyamba munali anthu a mitundu ina mwakuthupi.+ Anthu otchedwa “odulidwa,” amene anadulidwa mwakuthupi ndi manja,+ anali kukutchani “osadulidwa.” 12 Muzikumbukiranso kuti pa nthawi imene ija munali opanda Khristu,+ otalikirana+ ndi mtundu wa Isiraeli komanso alendo osadziwika pa mapangano a lonjezolo.+ Munalibe chiyembekezo+ ndipo inu munalibe Mulungu m’dzikoli.+ 13 Koma tsopano mogwirizana ndi Khristu Yesu, inu amene pa nthawi ina munali kutali, mwakhala pafupi chifukwa cha magazi+ a Khristu. 14 Pakuti iye ndiye mtendere wathu,+ amene analumikiza mbali ziwiri+ kukhala imodzi,+ ndi kugwetsa khoma+ lowalekanitsa limene linali pakati pawo.+ 15 Ndi thupi lake,+ anathetsa chidani chimene chinalipo,+ chimene ndi Chilamulo chokhala ndi malamulo operekedwa monga malangizo.+ Anachithetsa kuti mogwirizana ndi iye, alenge munthu mmodzi watsopano+ kuchokera ku magulu awiri a anthu,+ ndi kukhazikitsa mtendere. 16 Ndiponso kuti kudzera mwa mtengo wozunzikirapo*+ ayanjanitse+ magulu awiri a anthuwo kwa Mulungu, ndipo anthuwo akhale thupi limodzi,+ chifukwa anali atapheratu chidanicho+ kudzera mwa iye mwini. 17 Chotero iye anabwera n’kulengeza uthenga wabwino wa mtendere+ kwa inuyo, inu akutali, ndipo analengezanso mtendere kwa apafupi,+ 18 chifukwa kudzera mwa iye, magulu onse awirife+ tingathe kufikira+ Atate mwa mzimu umodzi.+
19 Chotero, simulinso anthu osadziwika+ kapena alendo m’dziko la eni,+ koma ndinu nzika+ zinzawo za oyerawo,+ ndipo ndinu a m’banja+ la Mulungu. 20 Mwamangidwa pamaziko+ a atumwi+ ndi aneneri,+ ndipo Khristu Yesuyo ndiye mwala wapakona wa mazikowo.+ 21 Mogwirizana ndi iye, nyumba yonse, pokhala yolumikizana bwino,+ ikukula kukhala kachisi woyera wa Yehova.+ 22 Mogwirizana ndi iye,+ inunso mukumangidwa pamodzi kukhala malo oti Mulungu akhalemo mwa mzimu.+